Ngati njira imodzi yopititsila patsogolo nkhondo yothana ndi maukwati a ana mdera la Nyengere kwa mfumu yayikulu Mponela m’boma la Dowa bungwe la Golden Family Community-based lachisanu pa 28 march lapeleka nkhumba 30 komaso nkhuku 60 kwa magulu 10 a mmidzi yosiyanasiyana mderali.
Mkulu wabungweli Yamikani Chikho ndiye anatsogolela ntchito yogawa ziwetozi, yomwe ikulunjika maanja omwe ana awo alipachiopsezo choti akhoza kulowa m’banja akanali achichepere.
Polankhula ndi Dowa FM Online Chikho wati bungwe lake likukhulupilila kuti ziwetozi zisintha miyoyo yamawanja opindulawa omwe azigawana ziwetozi zikaswa ndiposo kuti makolowa azidzatha kugulitsako ziwetozi ndi kuthandizila maphuzilo a ana awo zomwe ati zizichepetsa chiwelengelo cha ana osiyila sukulu panjira kamba kaumphawi.
Ndipo mmawu ake mlembi wagulu wa kalabu ya Nyerere 2 Felix Chibwana wayamikila bungweli kamba kathandizoli ndipo wati ngati gulu ayesetsa kusamala ziwetozi zomwe akukhulupila kuti zisintha miyoyo wamaanja awo.
Bungwe la Golden Family Community-Based Organisation likugwira ntchito yothetsa ma ukwati a ana mdera la Nyengere yomwe inayamba January chaka chino ndipo ikuyembekezeka kudzatha December mchaka cha 2028.
Wolemba Boniface Selemani