Home Politics ANTHU A MMIDZI INA YA KWA MFUMU YAIKULU MPONELA AKONZA MISEU MMADERA AWO

ANTHU A MMIDZI INA YA KWA MFUMU YAIKULU MPONELA AKONZA MISEU MMADERA AWO

by Khumbo Chiudzu
0 comments

Phungu wa nyumba ya malamuro wadera lapakati pa boma la Dowa Darlington Harawa wati kukoza misewu ndi gwero lopititsa patsogolo ntchito za chitukuko kudera.

Harawa walankhula izi pa 29 March 2025 pomwe anatenga nawo mbali pa ntchito yokoza misewu yomwe midzi monga Tomasi, Sunduza, Chezini, Chulu 1, Chulu 2 komaso Thendo kwa mfumu yaikulu Mponela m’boma la Dowa.

Iye anatsindika kuti ntchito za malonda zimayenda bwino ngati misewu ili yolongosoka kudera.

Kumbali yake yemwe akudzapikisana nawo pa mpando wa khansala wadelali Kondwani Lisiya wati anachiona chinthu chofunikira kupeleka galimoto yake kuti ithandizile ntchito yotuta mchenga pa ntchitoyi ponena kuti ndi khumbo lake kuona delari likutukuka pa ntchito ya za malonda.

Lisiya wati masomphenya ake otengapo gawo pa ntchito zachitukuko sakuthela pomwepa koma kuonetsetsaso kuti miyoyo ya anthu okhala kumidzi yosiyanasiyana ikutukuka pankhani ya zachuma pomwe wati akangosankhidwa pa udindowu adzaonetsetsa kuti anthu ali ndi mpamba oyambila ma bizinesi awo ndikumakhala odzidalila pa nkhani ya zachuma.

Wolemba Chifuniro Smoke

You may also like

Leave a Comment

Dowa Community Radio is a community-based radio station established in 2020 to be used as a tool of communication in Dowa district and surrounding areas to facilitate issues of Education, gender-based violence, culture, child trafficking, Agriculture, Climate change and environment, transparency and accountability, sports, community self reliance, and many more.

Newsletter

Subscribe my Newsletter for new blog posts, tips & new photos. Let's stay updated!

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00