Home Uncategorized BUNGWE LA NUDINGA HANDS FOUNDATION LATHANDIZA ANA OSOWA KU DOWA

BUNGWE LA NUDINGA HANDS FOUNDATION LATHANDIZA ANA OSOWA KU DOWA

by Khumbo Chiudzu
0 comments

Bungwe la Nudinga Hands Foundation lapeleka thandizo la zovala zakusukulu komaso katundu wina monga shuga, sopo ndi makope kwa ana asukulu omwe ndiosowa m’mapezedwe.

Polankhula ndi Dowa FM Online m’mudzi mwa Kasalika, mfumu yaikulu Mponela m’boma la Dowa m’modzi mwa akuluakulu omwe amayendetsa bungweli a Nefitaly Damalankhunda ati cholinga chachikulu cha bungweli ndi kuonetsa kuti ana akupita kusukulu ndikutiso chiwerengero cha ana omwe akusiila sukulu panjila chachepa m’derali.

Iye anaonjezeraso kuti bungweli lapeleka thandizoli poonanso ndimomwe chiwelengelo cha ana omwe amakhala komaso kusiira sukulu panjila chikukwera kwambili m’derali.

Polankhula pa zokhudza thandizoli a sinyo gulupu Kasalika ati ndiokondwa ndi momwe bungweli laonetsela chidwi chopititsa patsogolo maphunziro potsindika kuti ndi masomphenya awo ndikuona mwana wa derali akupita patali ndi maphunziro ndipo apempha bungweli kuti lisasiyile panjila ntchitoi yomwe ikugwilizana ndi masomphenya a dziko lino achaka cha 2063.

Wolemba Chifuniro Smoke

You may also like

Leave a Comment

Dowa Community Radio is a community-based radio station established in 2020 to be used as a tool of communication in Dowa district and surrounding areas to facilitate issues of Education, gender-based violence, culture, child trafficking, Agriculture, Climate change and environment, transparency and accountability, sports, community self reliance, and many more.

Newsletter

Subscribe my Newsletter for new blog posts, tips & new photos. Let's stay updated!

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00