BWALO LA CHAMPION KU MPONELA LASANKHIDWA KUCHITITSA MASEWERO A TNM SUPER LEAGUE

Bwalo la Champion ku Mponela boma la Dowa lili gulu limodzi mwa mabwalo 11 omwe komiti yoona za ndondomeko yamakono yoyendetsa masewero a mpira wamiyendo yapadera yotchedwa, Football Association Of Malawi (FAM)Club Licensing First Instance body, mchingerezi yapereka kuti atha kuchititsa masewero a TNM Super League ya chaka chino.

Bungwe la FAM lidayendera mabwalo okwana 16 mmiyezi ya January ndi March chaka chino.

Mabwalo a Balaka ndi Civo alephera mayeso kuti sangachititse masewero.

Mabwalo omwe avomerezedwa ndi ,Rumphi,(Rumphi) Chitowe (Nkhotakota), Champion (Dowa), Silver (Lilongwe), Nankhaka (Lilongwe), Dedza(Dedza), Kamuzu (Blantyre), Mulanje, Karonga, Mzuzu komanso Bingu mu nzinda wa Lilongwe.

Bwalo la Dimba lomwe lili ku Mchinji komaso Mpira lomwe lili ku Blantyre ayikidwa kaye padera kuti ali ndi zochepa zoyenera kukonza ndipo ngati zitakonzedwe mwachangu mabwalowa ayamba kugwira ntchito.

Wolemba: Andrew Mdzumira

Related posts

ORANT CHARITIES AFRICA AND OPULENCE MALAWI SIGNS A MEMORANDUM OF UNDERSTANDING IN DOWA

MAN ARRESTED FOR MURDERING HIS FRIEND IN DOWA

MAGULU KHUMI ALANDIRA ZIWETO ZOTHANDIZIRA KUTHETSA MAUKWATI A ANA KU DOWA